Hebrews 1:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake nkale lonse Mulungu sadauzepo mngelo aliyense kuti, “Iwe ndiwe mwana wanga, Ine lero ndakubala.” Mulungu sadakambepo za mngelo aliyense kuti, “Ine ndidzakhala bambo wake, iye adzakhala mwana wanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti kwa mngelo uti anati nthawi iliyonse, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero Ine ndakubala Iwe? Ndiponso, Ine ndidzakhala kwa Iye Atate, ndipo Iye adzakhala kwa Ine Mwana?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi ndi kwa mngelo uti, kumene Mulungu anati, “Iwe ndiwe mwana wanga; Ine lero ndakhala Atate ako.” Kapena kunenanso kuti, “Ine ndidzakhala abambo ake; iye adzakhala mwana wanga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti kwa mngelo uti anati nthawi iri yonse, Iwe ndiwe Mwana wanga, Lero ine ndakubala Iwe? ndiponso, Ine ndidzakhala kwa iye Atate, Ndipo iye adzakhala kwa ine Mwana?