Hebrews 1:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudakonda chilungamo nkudana ndi zosalungama. Nchifukwa chake Ine, Mulungu wanu, ndakukwezani nkukudzozani ndi mafuta osonyeza chimwemwe, kupambana anzanu ena onse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwakonda chilungamo, ndi kudana nacho choipa; mwa ichi Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wakudzozani ndi mafuta a chikondwerero chenicheni koposa anzanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa; Nʼchifukwa chake, Mulungu wanu wakukwezani kuposa anzanu pokudzozani mafuta osonyeza chimwemwe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwakonda cilungamo, ndi kudana naco coipa; Mwa ici Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wakudzozani Ndi mafuta a cikondwerero ceni ceni koposa anzanu.