Hebrews 10:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Malamulo a Mose ndi chithunzi chabe cha madalitso amene alikudza, osati madalitso enieniwo. Ngakhale nsembe zimodzimodzi zimaperekedwa kosalekeza chaka ndi chaka, Malamulowo sangathe konse mwa nsembezo kuŵasandutsa angwiro anthu oyandikira pamenepo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti chilamulo, pokhala nao mthunzi wa zokoma zilinkudza, osati chifaniziro chenicheni cha zinthuzo, sichikhozatu, ndi nsembe zomwezi chaka ndi chaka, zimene azipereka kosalekeza, kuwayesera angwiro iwo akuyandikira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Malamulo ndi chithunzithunzi cha zinthu zabwino zimene zikubwera, osati madalitso enieniwo. Pa chifukwa chimenechi sizingatheke konse kuti nsembe zimodzimodzi, zoperekedwa kawirikawiri, kosalekeza ndi chaka ndi chaka, kuti nʼkusandutsa angwiro amene amabwera kudzapembedza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mthunzi wa zokoma zirinkudza, osati cifaniziro ceni ceni ca zinthuzo, sicikhozatu, ndi nsembe zomwezi caka ndi caka, zimene azipereka kosalekeza, kuwayesera angwiro iwo akuyandikira.