Hebrews 10:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu opembedza Mulungu aja akadayeretsedwa kwathunthu, sibwenzi mtima wao ukuŵatsutsabe, ndipo akadaleka kumapereka nsembe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakadapanda kutero, kodi sakadaleka kuzipereka, chifukwa otumikirawo sakadakhala nacho chikumbu mtima cha machimo, popeza adayeretsedwa kamodzi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati zikanamatero iwowo akanasiya kupereka nsembezo. Pakuti opembedzawo akanamayeretsedwa kamodzi kokha, sibwenzi chikumbumtima chawo chikuwatsutsabe chifukwa cha machimo awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakadapanda kutero, kodi sakadaleka kuzipereka, cifukwa otumikirawo sakadakhala naco cikumbu mtima ca macimo, popeza adayeretsedwa kamodzi?