Hebrews 10:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanji tsono munthu wonyoza Mwana wa Mulungu, munthu woyesa chinthu chachabe magazi achipangano amene adamuyeretsa, munthu wonyoza Mzimu wotipatsa madalitso a Mulungu! Chilango cha munthu wotere chidzakhala choopsa kopambana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo mutani, kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene anapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa chipangano umene anayeretsedwa nao chinthu wamba, nachitira chipongwe Mzimu wa chisomo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koposa kotani nanga ululu wachilango chimene adzalandire munthu amene amapeputsa Mwana wa Mulungu, amene amayesa magazi a pangano, amene anamuyeretsa, kukhala chinthu chodetsedwa, ndi kunyoza Mzimu wachisomo?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo mutani, kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene anapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa cipangano umene anayeretsedwa nao cinthu wamba, z nacitira cipongwe Mzimu wa cisomo;