Hebrews 10:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake pamene Khristu adadza pansi pano, adati, “Inu Mulungu simudafune nsembe kapena zopereka, koma thupi mudandikonzera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwa ichi polowa m'dziko lapansi, anena, Nsembe ndi chopereka simunazifuna, koma thupi munandikonzera Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake Khristu atabwera pa dziko lapansi anati, “Simunafune nsembe kapena zopereka, koma thupi munandikonzera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwa ici polowa m'dziko lapansi, anena, Nsembe ndi copereka simunazifuna, Koma thupi munandikonzera Ine.