Hebrews 10:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero poyamba adati, “Nsembe kapena zopereka, nsembe zopsereza kwathunthu kapenanso nsembe zoperekera machimo, simudazifune ndipo simudakondwere nazo.” Zimenezi nzimene Malamulo adaanena kuti ziperekedwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakunena pamwamba apa, kuti, Nsembe ndi zopereka ndi nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simunazifuna, kapena kukondwera nazo (zimene ziperekedwa monga mwa lamulo),
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Poyamba Iye anati, “Nsembe kapena zopereka zopsereza ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo, Inu simunazifune kapena kukondwera nazo.” Ngakhale kuti Malamulo ndiye amanena kuti ziperekedwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakunena pamwamba apa, kuti, Nsembe ndi zopereka ndi nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa macimo simunazifuna, kapena kukondwera nazo (zimene ziperekedwa monga mwa lamulo),