Hebrews 11:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onseŵa adasunga chikhulupiriro chao mpaka kufa. Sadalandire zimene Mulungu adaaŵalonjeza, koma adangoziwonera chapatali ndi kuzikondwerera. Adaavomera kuti pansi pano analidi alendo osakhazikika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwo onse adamwalira m'chikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adawaona ndi kuwalankhula kutali, navomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onsewa anakhalabe mwachikhulupiriro mpaka anafa. Iwo sanalandire zimene Mulungu anawalonjeza; iwo anangozionera chapatali ndi kuzilandira. Ndipo iwo anavomereza kuti analidi alendo ndi osakhazikika pa dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwo onse adamwalira m'cikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adawaona ndi kuwalankhula kutali, nabvomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.