Hebrews 11:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pokhala ndi chikhulupiriro, Abrahamu, pamene Mulungu adamuyesa, adapereka Isaki ngati nsembe. Ngakhale anali munthu woti Mulungu adaampatsa lonjezo, adakhala wokonzeka kupereka ngati nsembe mwana wake mmodzi yekhayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poyesedwa, anapereka nsembe Isaki, ndipo iye mene adalandira malonjezano anapereka mwana wake wayekha;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndi chikhulupiriro Abrahamu, Mulungu atamuyesa, anapereka Isake ngati nsembe. Ngakhale anali munthu woti Mulungu anamulonjeza, anakhala wokonzeka kupereka nsembe mwana wake mmodzi yekhayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi cikhulupiriro Abrahamu, poyesedwa, anapereka nsembe Isake, ndipo iye amene adalandira malonjezano anapereka mwana wace wayekha;