Hebrews 11:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abrahamu ankakhulupirira kuti Mulungu nkuukitsa munthu kwa akufa. Tsono tingathe kunena mofanizira kuti adamlandiranso Isakiyo ngati wouka kwa akufa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
poyesera iye kuti Mulungu ngwokhoza kuukitsa, ngakhale kwa akufa; kuchokera komwe, pachiphiphiritso, anamlandiranso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abrahamu amazindikira kuti Mulungu angathe kuukitsa akufa, ndipo tingathe kunena mofanizira kuti iye analandiranso Isake ngati wouka kwa akufa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
poyesera iye kuti Mulungu ngwokhoza kuukitsa, ngakhale kwa akufa; kucokera komwe, paciphiphiritso, anamlandiranso.