Hebrews 11:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pokhala ndi chikhulupiriro, atabadwa Mose, makolo ake adamubisa miyezi itatu, poona kuti mwana waoyo anali wokongola. Sadaope konse lamulo lamphamvu la mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi chikhulupiriro Mose, pobadwa, anabisidwa miyezi itatu ndi akum'bala, popeza anaona kuti ali mwana wokongola; ndipo sanaopa chilamuliro cha mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndi chikhulupiriro Mose atabadwa makolo ake anamubisa miyezi itatu, chifukwa iwo anaona kuti mwanayo anali wokongola ndipo sanaope konse lamulo la mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi cikhulupiriro Mose, pobadwa, anabisidwa miyezi itatu ndi akumbala, popeza anaona kuti ali mwana wokongola; ndipo sanaopa cilamuliro ca mfumu.