Hebrews 11:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pokhala ndi chikhulupiriro, Mose adachoka ku Ejipito, osaopa ukali wa mfumu, popeza kuti ankapirira ngati munthu woona Mulungu wosaonekayu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi chikhulupiriro anasiya Ejipito, wosaopa mkwiyo wa mfumu; pakuti anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndi chikhulupiriro anachoka ku Igupto wosaopa ukali wa mfumu. Iye anapirira chifukwa anamuona Mulungu amene ndi wosaonekayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi cikhulupiriro anasiya Aigupto, wosaopa mkwiyo wa mfumu; pakuti anapirira molimbika monga ngari kuona wosaonekayo.