Hebrews 11:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ena adazimitsa moto waukali, ndipo ena adapulumuka, osaphedwa ndi lupanga. Anali ofooka, koma adalandira mphamvu. Adasanduka ngwazi pa nkhondo, nathamangitsa magulu a ankhondo a adani ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nazima mphamvu ya moto, napulumuka lupanga lakuthwa, analimbikitsidwa pokhala ofooka, anakula mphamvu kunkhondo, anapirikitsa magulu a nkhondo yachilendo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
anazimitsa moto waukali, ndipo anapulumuka osaphedwa ndi lupanga. Anali ofowoka koma analandira mphamvu; anasanduka amphamvu pa nkhondo, nathamangitsa magulu a ankhondo a adani awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
12 nazima mphamvu ya moto, 13 napulumuka lupanga lakuthwa, 14 analimbikitsidwa pokhala ofok a, anakula mphamvu kunkhondo, 15 anapitikitsa magulu a nkhondo yacilendo.