Hebrews 11:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pokhala ndi chikhulupiriro, Enoki adatengedwa kupita Kumwamba, osafa konse. Sadapezekenso, popeza kuti Mulungu adamtenga. Malembo amamchitira umboni kuti asanatengedwe, anali wokondweretsa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi chikhulupiriro Enoki anatengedwa kuti angaone imfa; ndipo sanapezeka, popeza Mulungu adamtenga: pakuti asanamtenge, anachitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndi chikhulupiriro Enoki anatengedwa wamoyo, motero iye sanalawe imfa; sanapezeke chifukwa Mulungu anamutenga. Pakuti asanatengedwe anayamikiridwa kuti ankakondweretsa Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi cikhulupiriro Enoke anatengedwa kuti angaone imfa; ndipo sanapezeka, popeza Mulungu adamtenga: pakuti asanamtenge, anacitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu;