Hebrews 11:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pokhala ndi chikhulupiriro, Abrahamu adamvera pamene Mulungu adamuitana kuti apite ku dziko lina limene adaamlonjeza kuti lidzakhala lake. Ngakhale sankadziŵa kumene ankapita, adapitabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka kumalo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo anatuluka wosadziwa kumene akamukako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndi chikhulupiriro Abrahamu atayitanidwa kuti apite ku dziko limene anamulonjeza kuti lidzakhala lake, anamvera ndi kupita, ngakhale sanadziwe kumene ankapita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi cikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kuturuka kunka ku malo amene adzalandira ngati colowa; ndipo anaturuka wosadziwa kumene akamukako.