Hebrews 11:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pokhala ndi chikhulupiriro chomwecho, ankakhala ngati mlendo m'dzikolo limene Mulungu adaamlonjeza. Ankakhala m'mahema pamodzi ndi Isaki ndi Yakobe, amene nawonso anali atalandira lonjezo lomwelo la Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi chikhulupiriro anakhala mlendo kudziko la lonjezano, losati lake, nakhalira m'mahema pamodzi ndi Isaki ndi Yakobo, olowa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwelo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndi chikhulupiriro chomwecho anakhala ngati mlendo mʼdziko lija limene Mulungu anamulonjeza. Anakhala mʼmatenti monganso anachitira Isake ndi Yakobo, amene nawonso analonjezedwanso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi cikhulupiriro anakhala mlendo ku dziko la lonjezano, losati lace, nakhalira m'mahema pamodzi ndi Isake ndi Yakobo, olowa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwelo;