Hebrews 12:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono popeza ifenso tazunguliridwa ndi gulu lalikulu la mboni, tiyeni titaye chilichonse chimene chimatitchinga, makamaka tchimo limene limatikola mosavuta, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukuru wotere wa mboni, titaye colemetsa ciri conse, ndi cimoli Iimangotizinga, ndipo tithamange mwacipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womariza wa cikhulupiriro cathu,