Hebrews 12:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma Iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa chiyero chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abambo athu ankatilanga kwa kanthawi kochepa monga amaonera kufunika kwake, koma Mulungu amatilanga kuti tipindule, kuti tikhale oyera mtima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa ciyero cace.