Hebrews 12:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondwetsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Palibe chilango chimene chimaoneka kuti ndi chabwino pa nthawiyo, komatu chowawa. Koma pambuyo pake, chimabweretsa chipatso chachilungamo ndi mtendere kwa iwo amene aleredwa mwa njira imeneyi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Chango ciri conse, pakucitika, sicimveka cokondwetsa, komatu cowawa; koma citatha, cipereka cipatso ca mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa naco, ndico ca cilungamo.