Hebrews 12:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yangʼanitsitsani kuti wina aliyense asachiphonye chisomo cha Mulungu ndiponso kuti pasaphuke muzu wamkwiyo umene udzabweretsa mavuto ndi kudetsa ambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera cisomo ca Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungabvute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao;