Hebrews 12:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwafika kuchikondwerero kumene kwasonkhana ana oyamba a Mulungu, amene maina ao adalembedwa Kumwamba. Mwafika kwa Mulungu, mweruzi wa anthu onse, ndiponso kwa mizimu ya anthu olungama, amene Mulungu waŵasandutsa angwiro kwenikweni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kwa msonkhano wa onse ndi Mpingo wa obadwa oyamba olembedwa m'Mwamba, ndi kwa Mulungu Woweruza wa onse, ndi kwa mizimu ya olungama oyesedwa angwiro,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwafika mu mpingo wa ana oyamba kubadwa, amene mayina awo analembedwa kumwamba. Inu mwafika kwa Mulungu, woweruza anthu onse, ndiponso kwa mizimu ya anthu olungama ndi osandutsidwa kukhala angwiro.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kwa msonkhano wa onse ndi Mpingo wa obadwa oyamba olembedwa m'Mwamba, ndi kwa Mulungu Woweruza wa onse, ndi kwa mizimu ya olungama oyesedwa angwiro,