Hebrews 12:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chenjerani tsono kuti musakane kumvera amene akulankhula nanu. Anthu amene adakana kumvera iye uja amene adaaŵachenjeza pansi pano, sadapulumuke ku chilango ai. Nanji tsono ifeyo, tidzapulumuka bwanji ngati timufulatira wotilankhula kuchokera Kumwambaku?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Penyani musakane wolankhulayo. Pakuti ngati iwowa sanapulumuka, pomkana Iye amene anawachenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, odzipatulira kwa Iye wa Kumwamba;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chenjerani kuti musakane kumvera amene akuyankhula nanu. Anthu amene anakana kumvera iye amene anawachenjeza uja pa dziko lapansi pano, sanapulumuke ku chilango ayi, nanga tsono ife tidzapulumuka bwanji ngati tikufulatira wotichenjeza wochokera kumwamba?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Penyani musakane wolankhulayo. Pakuti ngati iwowa sanapulumuka, pomkana iye amene anawacenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, odzipatulira kwa iye wa Kumwamba;