Hebrews 12:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mau akuti “Kamodzi kenanso” akuwonetsa poyera kuti zolengedwa zonse zogwedezeka zidzachotsedwa, kuti zinthu zosagwedezeka zidzakhalitse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ichi, chakuti kamodzinso, chilozera kusuntha kwake kwa zinthu zogwedezeka, monga kwa zinthu zolengedwa, kuti zinthu zosagwedezeka zikhale.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mawu akuti, “Kamodzi kenanso,” akuonetsa kuchotsedwa kwa zimene zitha kugwedezeka, zonse zolengedwa, kotero kuti zimene sizingatheke kugwedezeka zitsale.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ici, cakuti kamodzinso, cilozera kusuntha kwace kwa zinthu zogwedezeka, monga kwa zinthu zolengedwa, kuti zinthu zosagwedezeka zikhale.