Hebrews 12:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwaiŵala kodi mau olimbitsa mtima aja, amene Mulungu amakulankhulani ngati ana ake? Mauwo ndi aŵa: “Mwana wanga, usanyozere malango a Ambuye, kapena kutaya mtima pamene Iwo akudzudzula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo mwaiwala dandauliro limene linena nanu monga ndi ana, Mwana wanga, usayese chopepuka kulanga kwa Ambuye, kapena usakomoke podzudzulidwa ndi Iye;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi mwayiwala mawu olimbitsa mtima aja, amene Mulungu anayankhula kwa inu ngati ana ake? Mawuwo ndi awa: “Mwana wanga, usapeputse kulanga kwa Ambuye ndipo usataye mtima pamene akukudzudzula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo mwaiwala dandauliro limene linena nanu monga ndi ana, Mwana wanga, usayese copepuka kulanga kwa Ambuye, Kapena usakomoke podzudzulidwa ndilye;