Hebrews 12:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muzipirira masautso kuti muphunzirepo makhalidwe oyenera. Mulungu amakutengani ngati ana ake m'zochita zake zonse. Kodi nkale lonse analipo mwana amene bambo wake sadamlange?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukapirira kufikira kulangidwa Mulungu achitira inu monga ngati ana; pakuti mwana wanji amene atate wake wosamlanga?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene mukupirira masautso monga chilango, Mulungu achitira inu monga ana ake. Kodi ndi mwana wotani amene abambo ake samulanga?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukapirira kufikira kulangidwa Mulungu acitira inu monga ngati ana; pakuti mwana wanji amene atate wace wosamlanga?