Hebrews 13:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkulu wa ansembe wachiyuda amaloŵa ndi magazi a nyama ku Malo Opatulika kuti magaziwo akhale nsembe yopepesera machimo. Koma nyama yeniyeniyo amaiwotchera kunja kwa misasa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti matupi a nyama zija, mwazi wa izo umatengedwa, ndi mkulu wa ansembe kulowa m'malo opatulidwa, chifukwa cha zoipa, amatenthedwa kunja kwa tsasa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkulu wa ansembe amatenga magazi kukapereka nsembe chifukwa cha machimo, koma nyamayo imawotchedwa kunja kwa msasa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti matupi a nyama zija, mwazi wa izo umatengedwa ndi mkulu wa ansembe kulowa m'malo opatulidwa, cifukwa ca zoipa, amatenthedwa kunja kwa tsasa.