Hebrews 13:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muzimvera atsogoleri anu ndi kuŵagonjera. Iwo sapumulira konse poyang'anira moyo wanu, pakuti adzayenera kufotokoza za ntchito yao pamaso pa Mulungu. Mukaŵamvera, adzagwira ntchito yaoyo mokondwa osati monyinyirika, kupanda kutero ndiye kuti kwa inuyo phindu palibe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muzimvera atsogoleri anu ndi kugonjera ulamuliro wawo, iwo amakuyangʼanirani monga anthu amene adzayenera kufotokoza za ntchito yawo pamaso pa Mulungu. Muziwamvera kuti agwire ntchito yawo ndi chimwemwe osati molemedwa pakuti izi sizingakupindulireni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akacite ndi cimwemwe, osati mwacisoni: pakuti ici sicikupindulitsani inu.