Hebrews 2:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja Mulungu amene ndi Mlengi wa zonse ndipo zonse zimalinga kwa Iye, adafuna kufikitsa ana ake ambiri ku ulemerero. Tsono kudaamuyenera kuti mwa njira ya zoŵaŵa, amsandutse Yesu mtsogoleri wangwiro woŵatsogolera ku chipulumutso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti kunamuyenera Iye amene zonse zili chifukwa cha Iye, ndi zonse mwa Iye, pakutenga ana ambiri alowe ulemerero, kumkonza wamphumphu mtsogoleri woyamba wa chipulumutso chao mwa zowawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu amene analenga zinthu zonse ndipo zinthu zonse zilipo chifukwa cha Iye ndi mwa Iye, anachiona choyenera kubweretsa ana ake ambiri mu ulemerero. Kunali koyenera kudzera mʼnjira ya zowawa, kumusandutsa Yesu mtsogoleri wangwiro, woyenera kubweretsa chipulumutso chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti kunamuyenera iye amene zonse ziri cifukwa ca iye, ndi zonse mwa Iye, pakutenga ana ambiri alowe ulemerero, kumkonza wamphumphu mtsogoleri woyamba wa cipulumutso cao mwa zowawa.