Hebrews 2:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake adaayenera kusanduka wofanafana ndi abale ake pa zonse, kuti akhale mkulu wa ansembe onse wachifundo ndi wokhulupirika potumikira Mulungu, ndipo kuti pakutero achotse machimo a anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m'zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha zimenezi, Iye anayenera kukhala wofanana ndi abale ake pa zonse, kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika potumikira Mulungu, kuti potero achotse machimo a anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m'zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wadfundo ndi wokhulupirika m'zinthu zakwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu.