Hebrews 2:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu yemwe ankachitira umboni pakuchita zizindikiro, zinthu zozizwitsa ndi ntchito zamphamvu zamitundumitundu, ndi pakuŵagaŵira mphatso za Mzimu Woyera monga momwe Iye ankafunira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pochita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundumitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu anachitiranso umboni pochita zizindikiro, zinthu zodabwitsa ndi zamphamvu zamitundumitundu ndi powapatsa mphatso za Mzimu Woyera monga mwachifuniro chake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pocita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikilo, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundu mitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa cifuniro cace.