Hebrews 3:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja timasanduka anzake a Khristu, malinga tikasunga kwenikweni mpaka potsiriza kulimba mtima kumene tinali nako poyamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pakuti takhala ife olandirana ndi Khristu, ngatitu tigwiritsa chiyambi cha kutama kwathu kuchigwira kufikira chitsiriziro;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti timakhala anzake a Khristu, ngati tigwiritsitsa mpaka potsiriza chitsimikizo chimene tinali nacho pachiyambi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti takhala ife olandirana ndi Kristu, ngatitu tigwiritsa ciyambi ca kutama kwathu kucigwira kufikira citsiriziro;