Hebrews 3:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Khristu anali wokhulupirika m'nyumba ya Mulungu ngati mwana wolamulira pa zonse za m'nyumba mwakemo. Ndipo nyumba yakeyo ndife, ngati tiika mphamvu pa kulimba mtima ndi kunyadira zimene tikuziyembekeza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma Khristu monga mwana, wosunga nyumba yake; ndife nyumba yake, ngati tigwiritsa kulimbika mtima ndi kudzitamandira kwa chiyembekezocho, kuchigwira kufikira chitsiriziro.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Khristu ndi wokhulupirika monga mwana pa nyumba ya Mulungu. Ndipo ndife nyumba yake ngati tipitirire kulimbika mtima ndi kunyadira zomwe tikuyembekerazo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma Kristu monga mwana, wosunga nyumba yace; ndife nyumba yace, ngati tigwiritsa kulimbika mtima ndi kudzitamandira kwa ciye-I mbekezoeo, kucigwira kufikira citsiriziro.