Hebrews 4:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti sitili ndi Mkulu wa ansembe amene sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofowoka zathu. Koma tili naye amene anayesedwa mʼnjira zonse monga ife, koma sanachimwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti sitiri naye mkulu wa ansembe wosatha kumva cifundo ndi zofoka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda ucimo.