Hebrews 4:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja ifenso tidaumva Uthenga Wabwino, monga iwo aja. Koma iwowo sadapindule nawo mau olalikidwawo, popeza kuti adangoŵamva, koma osaŵakhulupirira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti kwa ifenso walalikidwa Uthenga Wabwino, monganso kwa iwo; koma iwowa sanapindula nao mau omvekawo, popeza sanasanganizika ndi chikhulupiriro mwa iwo amene adawamva.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Uthenga Wabwino unalalikidwa kwa ife, monganso iwo aja; koma iwo sanapindule nawo uthengawo chifukwa anangomva koma osakhulupirira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti kwa ifenso walalikidwa Uthenga Wabwino, monganso kwa iwo; koma iwowa sanapindula nao mau omvekawo, popeza sanasanganizika ndi cikhulupiriro mwa iwo amene adawamva.