Hebrews 4:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ife okhulupirirafe tikuloŵamo mu mpumulowo. Paja Mulungu adaanena kuti, “Ndili wokwiya ndidalumbira kuti, ‘Sadzaloŵa konse mu mpumulo umene ndidaŵakonzera.’ ” Adaanena zimenezi, ngakhale anali atatsiriza ntchito zake zonse za kulenga dziko lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza ife amene takhulupirira tilowa mpumulowo, monga momwe ananena, Monga ndalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mpumulo wanga. Zingakhale ntchitozo zidatsirizika kuyambira kuzika kwa dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono ife amene takhulupirira talowa mu mpumulo, monga momwe Mulungu akunenera kuti, “Ndili wokwiya ndinalumbira kuti, ‘Iwo sadzalowa konse mu mpumulo wanga.’ ” Ananena zimenezi ngakhale anali atatsiriza kale ntchito yolenga dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza ife amene takhulupira tilowa mpumulowo, monga momwe ananena, Monga ndalumbira mu mkwiyowanga, Ngati adzalowa mpumulo wanga: zingakhale nebitozo zidatsirizika kuyambira kuzika kwa dziko lapansi.