Hebrews 4:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Mulungu adaikanso tsiku lina, lotchedwa kuti “Lero”. Patapita nthaŵi yaitali Mulungu adalankhula za tsiku lomweli kudzera mwa Davide ponena mau aja tatchula kaleŵa, akuti, “Lero, mukamva mau a Mulungu, musaumitse mitima yanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
alangizanso tsiku lina, ndi kunena m'Davide, itapita nthawi yaikulu yakuti, Lero, monga kwanenedwa kale, Lero ngati mudzamva mau ake, musaumitse mitima yanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake Mulungu anayikanso tsiku lina limene analitcha “Lero.” Patapita nthawi yayitali Iye anayankhula za tsiku lomweli kudzera mwa Davide, monga ndinanena kale kuti, “Lero mukamva mawu ake, musawumitse mitima yanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
alangizanso tsiku lina, ndi kunena m'Davide, itapita nthawi yaikuru yakuti, Lero, monga kwanenedwakale, Lero ngati mudzamva mau ace, Musaumitse mitima yanu.