Hebrews 5:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa pakati pa anthu, namuika kuti aziŵaimirira pamaso pa Mulungu. Ntchito yake nkupereka mphatso ndi nsembe chifukwa cha machimo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mkulu wa ansembe aliyense, wotengedwa mwa anthu, amaikika chifukwa cha anthu m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke mitulo, ndiponso nsembe chifukwa cha machimo:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa kuchokera pakati pa anthu ndipo amayikidwa kuti aziwayimirira pamaso pa Mulungu, kuti azipereka mphatso ndi nsembe chifukwa cha machimo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mkulu wa ansembe ali yense, wotengedwa mwa anthu, amaikika cifukwa ca anthu m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke mitulo, ndiponso nsembe, cifukwa ca macimo: