Hebrews 5:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Lija nkale mukadayenera kukhala ophunzitsa anzanu, komabe nkofunika kuti wina akuphunzitseninso maphunziro oyamba enieni a mau a Mulungu. Nkofunikanso kukumwetsani mkaka, m'malo mwa kukupatsani chakudya cholimba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi, muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati chakudya chotafuna.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale kuti pa nthawi ino munayenera kukhala aphunzitsi, pakufunikabe munthu wina kuti abwerezenso kudzakuphunzitsani maphunziro oyambira a choonadi cha Mulungu. Ndinu ofunika mkaka osati chakudya cholimba!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi cifukwa ca nyengoyi, muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za ciyambidwe ca maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati cakudya cotafuna.