Hebrews 5:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Palibe munthu amadzitengera yekha ulemu wokhala mkulu wa ansembe onse, koma amachita kuitanidwa ndi Mulungu, monga momwe adaaitanidwira Aroni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo palibe munthu adzitengera ulemuwo mwini wake, komatu iye amene aitanidwa ndi Mulungu, monga momwenso Aroni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Palibe amene amadzipatsa yekha ulemu wotere, koma amachita kuyitanidwa ndi Mulungu monga momwe anayitanidwira Aaroni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo palibe munthu adzitengera ulemuwo mwini wace, komatu iye amene aitanidwa ndi Mulungu, monga momwenso Aroni.