Hebrews 5:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu, pa nthaŵi imene anali munthu pansi pano, mofuula ndi molira misozi, adapereka mapemphero ndi madandaulo kwa Mulungu, amene anali nazo mphamvu zompulumutsa ku imfa. Ndiye popeza kuti Yesu adaadzipereka modzichepetsa, Mulungu adamvera mapemphero ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu, pa nthawi imene anali munthu pa dziko lapansi pano, anapereka mapemphero ake ndi zopempha mofuwula ndi misozi kwa Iye amene akanamupulumutsa ku imfa, ndipo anamumvera chifukwa anagonjera modzipereka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ameneyo, m'masiku a thupi lace anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukuru ndi misozi kwa iye amene anakhoza kumpulumutsa iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,