Hebrews 6:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono tisangoima pa maphunziro oyamba enieni a Khristu. Tisachite kubwerezanso kuphunzitsa zomwe zili ngati maziko, monga za kutembenuka mtima kusiya ntchito zosapindulitsa moyo wosatha, za kukhulupirira Mulungu,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwa ichi, polekana nao mau a chiyambidwe cha Khristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu; osaikanso maziko a kutembenuka mtima kusiyana nazo ntchito zakufa, ndi a chikhulupiriro cha pa Mulungu,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono tiyeni tisangoyima pa maphunziro oyambirira enieni a Khristu koma tipitirire kuti mukule msinkhu. Tisaphunzitsenso zinthu zomwe zili ngati maziko, monga za kutembenuka mtima kusiya ntchito zosapindulitsa pa moyo wosatha, za kukhulupirira Mulungu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwa ici, polekana nao mau a ciyambidwe ca Kristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu; osaikanso maziko a kutembenuka mtima kusiyana nazo nchito zakufa, ndi a cikhulupiriro ca pa Mulungu,