Hebrews 6:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja Mulungu ngwolungama, sangaleke kusamalako za ntchito zanu, ndi chikondi chimene mudaamuwonetsa pakutumikira oyera ake, monga m'mene mukuchitirabe tsopano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu ndi wolungama, sangayiwale ntchito zanu ndi chikondi chanu chimene munamuonetsa pothandiza anthu ake monga mmene mukuchitirabe tsopano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala nchito yanu, ndi cikondico mudacionetsera ku dzina lace, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.