Hebrews 6:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero pali zinthu ziŵirizi, lonjezo ndi lumbiro, zimene sizingathe kusinthika, ndipo Mulungu sanganamirepo. Mwa zimenezi Mulungu adafuna kutilimbitsa mtima ife amene tidathaŵira kwa Iye, kuti tichigwiritse chiyembekezo chimene adatiikira pamaso pathu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sakhoza kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu anachita zinthu ziwiri, lonjezo ndi lumbiro, zimene sizingathe kusintha ndipo Mulungu sangathe kunama. Choncho Mulungu akutilimbikitsa mtima ife amene tinathawira kwa Iye kuti tichigwiritsitse chiyembekezo chimene tinalandira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sakhoza kunama, tikakhale naco coticenjeza colimba, ife amene tidathawira kucigwira ciyembekezo coikika pamaso pathu;