Hebrews 6:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu amene adataya chikhulupiriro chao, nkosatheka kuŵatsitsimutsa kuti atembenuke mtima. Iwowo kale Mulungu adaaŵaunikira, adaalaŵako mphatso yochokera Kumwamba, nkulandira nao Mzimu Woyera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anaunikidwa pa nthawi yake, nalawa mphatso ya Kumwamba, nakhala olandirana naye Mzimu Woyera,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼkosatheka kuwabwezanso anthu amene nthawi ina anawunikiridwa. Iwowa analawapo mphatso yochokera kumwamba, nʼkulandira nawo Mzimu Woyera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anaunikidwa pa nthawi yace, nalawa mphatso ya Kumwamba, nakhala olandirana naye Mzimu Woyera,