Hebrews 7:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abrahamu adampatsa chigawo chachikhumi cha zonse zimene adaafunkha. Potsata tanthauzo la dzina lake, choyamba Melkizedeki ndi “Mfumu ya chilungamo,” pambuyo pake ndi “Mfumunso ya Salemu,” ndiye kuti, “Mfumu ya Mtendere”.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amenenso Abrahamu anamgawira limodzi la magawo khumi la zonse (ndiye posandulika, poyamba ali mfumu ya chilungamo, pameneponso mfumu ya Salemu, ndiko, mfumu ya mtendere;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Abrahamu anamupatsa chakhumi cha zonse anafunkha. Choyamba dzina la Melikizedeki likutanthauza, “Mfumu ya chilungamo,” kenakanso, “Mfumu ya Salemu,” kutanthauza, “Mfumu ya mtendere.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amenenso Abrahamu anamgawira limodzi la magawo khumi la zonse (ndiye posandulika, poyamba ali Mfumu ya cilungamo, pameneponso Mfumu ya Salemu, ndiko, Mfumu ya mtendere;