Hebrews 7:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake angathe kuŵapulumutsa kwathunthu anthu amene akuyandikira kwa Mulungu kudzera mwa Iye, pakuti Iyeyo ali ndi moyo nthaŵi zonse kuti aziŵapempherera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chake Iye amapulumutsa kwathunthu amene amabwera kwa Mulungu kudzera mwa Iyeyo. Iye ali ndi moyo nthawi zonse kuti adziwapempherera iwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kucokera komwekoakhoza kupulumutsa konse konse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa iye, popeza ali nao moyo wace cikhalire wa kuwapembedzera iwo.