Hebrews 7:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono padaafunika kuti tikhale naye wotere mkulu wa ansembe onse: woyera mtima, wopanda choipa kapena chodetsa chilichonse, wosiyana ndi anthu ochimwa, ndiponso wokwezedwa kubzola zonse zakumwambaku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa, wakukhala wopitirira miyamba;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uyu ndi Mkulu wa ansembe amene tikumufuna chifukwa ndi woyera, wopanda choyipa kapena chodetsa chilichonse, wosiyana ndi anthu ochimwa, ndiponso wokwezedwa kuposa zonse zakumwambaku.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda coipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ocimwa, wakukhala wopitirira miyamba;