Hebrews 7:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu ameneyu sali ngati akulu a ansembe ena aja. Palibe chifukwa chakuti tsiku ndi tsiku azipereka nsembe poyamba chifukwa cha machimo ake, kenaka chifukwa cha machimo a anthu. Zimenezi adachitiratu kamodzi kokha, pakudzipereka yekha ngati nsembe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene alibe chifukwa cha kupereka nsembe tsiku ndi tsiku monga akulu a ansembe, yoyambira chifukwa cha zoipa za iwo eni, yinayi chifukwa cha zoipa za anthu; pakuti ichi anachita kamodzi, kwatha, podzipereka yekha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kusiyana ndi akulu a ansembe ena aja, Yesu sanafunike kupereka nsembe tsiku ndi tsiku poyamba chifukwa cha machimo ake, ndipo kenaka chifukwa cha machimo a anthu ena. Iye anadzipereka nsembe chifukwa cha machimo awo kamodzi kokha pamene anadzipereka yekha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amene alibe cifukwa ca kupereka nsembe tsiku ndi tsiku monga akulu a ansembe, yoyambira cifukwa ca zoipa za iwo eni, yinayi cifukwa ca zoipa za anthu; pakuti ici anacita kamodzi, kwatha, podzipereka yekha.