Hebrews 7:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Malamulo a Mose amaika anthu amene ali ndi zofooka, kuti akhale akulu a ansembe onse. Koma mau a lumbiro la Mulungu lija limene lidabwera pambuyo pa Malamulowo, adaika Mwana wake, amene wakhala wangwiro kwamuyaya kuti akhale mkulu wa ansembe onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti chilamulo chimaika akulu a ansembe anthu, okhala nacho chifooko; koma mau a lumbirolo, amene anafika chitapita chilamulo, aika Mwana, woyesedwa wopanda chilema kunthawi zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti lamulo limasankha anthu amene ndi ofowoka kukhala akulu a ansembe; koma lumbiro, lomwe linabwera pambuyo pa lamulo, linasankha Mwana, amene anapangidwa kukhala wangwiro kwamuyaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti cilamulo cimaika akuru a ansembe anthu, okhala naco cifoko; koma mau a lumbirolo, amene anafika citapita cilamulo, aika Mwana, woyesedwa wopanda cirema ku nthawi zonse.