Hebrews 7:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Za bambo wake kapena mai wake, kapena makolo ake, palibe chilichonse chidalembedwa. Chimodzimodzi za kubadwa kwake ndi imfa yakenso. Ali ngati Mwana wa Mulungu, akupitiriza kukhala wansembe mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
wopanda atate wake, wopanda amake, wopanda mawerengedwe a chibadwidwe chake, alibe chiyambi cha masiku ake kapena chitsiriziro cha moyo wake, wofanizidwa ndi Mwana wa Mulungu), iyeyu wakhala wansembe kosalekeza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Alibe abambo kapena mayi, alibe chiyambi kapena chitsiriziro cha moyo wake. Iye ali ngati Mwana wa Mulungu ndipo akupitirira kukhala wansembe wamuyaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
wopanda atate wace, wopanda amace, wopanda mawerengedwe a cibadwidwe cace, alibe ciyambi ca masiku ace kapena citsiriziro ca moyo wace, wofanizidwa ndi Mwana wa Mulungu), iyeyu wakhala wansembe kosalekeza.